Kanema wachidule
Where You Belong
2 minFHD
Sports·4 mwa 11Chidutswa 4 mwa 11
Where You Belong
On the field, there is nothing more important than the ball. The players will do everything to protect it and get the ball where it belongs. In the Game of Life, where do you belong?
MafunsoMafunso Ogwirizana
Funsani lanuMawu a Baibulo
GawaniPsalm 86:15
But You, O Lord, are a compassionate and gracious God, slow to anger, abounding in loving devotion and faithfulness.
Berean Standard Bible
Public Domain
Werengani zambiri...Lembalo la mawu
Chichewa (Chicheŵa)
Mpira nthawi zambili umapangidwa ndi chikopa, mphira ndi kusoka.
Siwapadera-dera.
Pali miyanda miyanda ya iwo m’dziko lirilonse la dziko lapansi.
Koma ukakhala mu bwalo la masewera...
sipamakhalanso chofunikira koposa.
Wosewera aliyenso mubwalomo
amafunitsitsa kudziwa kuti uli pati.
Aliyense kumasitandi akukuwa mwa chisangalalo.
Miyoyo yao itayiwalidwa,
zonse chifukwa cha mpira uwu.
Pamene wosewera wapetenga mpira,
chidwi chake chimakhala chosayimitsika.
Kwa iwo, mu mphindi iyi,
palibenso kena kalikonse, ndipo palibe wina aliyense, wofunikira zedi.
Sasamala kuti zimatengera mphamvu zochuluka bwanji,
kapena kuti angavulale patsogolo pake.
Amayimitsa mpira ndi matupi awo omwe.
Pali chinthu chimodzi chokha choyenera kuchita...
...kuponyera mpira kumene uyenere kupita.
Chimene chingakudabwitseni ndi ichi...
Umu ndi mmene Yesu amakuonerani.
Yesu amadziwa zonse za inu.
Ndipo amakulandirani mulimonsemo,
ndipo amafuna kukutetezani ndi kukusamalirani.
Yesu anaperekanso moyo wake pa chinthu chimodzi,
cholinga chamuyaya...
kuti mutha kukhala komwe muyenelera...
ku Nyumba.
Ndi Iye.
Komwe muyenera kukhala.
Mpira ukatha,
aliyense amachokamo mu sitediyamu.
Koma Yesu amakhala akudikilirabe.
Inuyo.
Yesu amakukondani.
Ndi chisankho chanu.
Muloleni akubweretseni kunyumba.